Foto do artista Hinos de Países

Hino do Malawi (Chichewa)

Hinos de Países


Mlungu dalitsani Malaŵi
Mumsunge m'mtendere
Gonjetsani adani onse
Njala, nthenda, nsanje
Lunzitsani mitima yathu
Kuti tisaope
Mdalitse mtsogoleri nafe
Ndi mayi Malaŵi

Malaŵi ndziko lokongola
La chonde ndi ufulu
Nyanja ndi mphepo ya m'mapiri
Ndithudi tadala
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu
N'mphatso zaulere
Nkhalango, madambo abwino
Ngwokoma Malaŵi

O ufulu tigwirizane
Kukweza Malaŵi
Ndi chikondi, khama, kumvera
Timutumikire
Pa nkhondo nkana pa mtendere
Cholinga n'chimodzi
Mayi, bambo, tidzipereke
Pokweza Malaŵi

Tradução Adicionar à playlist Tamanho Cifra Imprimir Corrigir